-
2 Mbiri 28:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Koma kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi. Iye anapita kukakumana ndi asilikali omwe ankabwerera ku Samariya nʼkuwauza kuti: “Tamverani! Yehova Mulungu wa makolo anu wapereka Ayuda mʼmanja mwanu+ chifukwa chakuti anawakwiyira kwambiri ndipo inuyo mwawapha mutakwiya ndipo mkwiyowo wafika mpaka kumwamba.
-