-
2 Mbiri 28:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Kenako amuna amene anachita kusankhidwa powatchula mayina ananyamuka nʼkutenga anthu ogwidwawo. Anthu onse amene sanavale* anawapatsa zovala kuchokera pa zinthu zimene zinabwera ndi asilikali zija. Anawapatsanso nsapato, chakudya, zakumwa komanso mafuta kuti adzole. Kuwonjezera pamenepo, aliyense amene ankayenda movutikira anamukweza pabulu. Atatero anawatenga nʼkupita nawo ku Yeriko, kumzinda wa mitengo ya kanjedza, kufupi ndi abale awo. Kenako iwo anabwerera ku Samariya.
-