23 Ahaziyo anayamba kupereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko+ imene inamugonjetsa,+ ndipo anati: “Milungu ya mafumu a Siriya ikuwathandiza, choncho ndipereka nsembe kwa milunguyi kuti inenso indithandize.”+ Koma milunguyo inachititsa kuti iye ndi Aisiraeli onse akumane ndi mavuto.