12 Zitatero Alevi anaimirira. Alevi ake anali Mahati mwana wa Amasai ndi Yoweli mwana wa Azariya, mbadwa za Kohati.+ Kuchokera kwa mbadwa za Merari,+ panali Kisi mwana wa Abidi ndi Azariya mwana wa Yehaleleli. Kuchokera kwa mbadwa za Gerisoni+ panali Yowa mwana wa Zima ndi Edeni mwana wa Yowa.