21 Iwo anabweretsa ngʼombe zamphongo 7, nkhosa zamphongo 7, ana a nkhosa amphongo 7 ndi mbuzi zamphongo 7 kuti azipereke nsembe yamachimo ya ufumuwo, ya malo opatulika ndi ya Yuda.+ Choncho Hezekiya anauza mbadwa za Aroni, zomwe zinali ansembe, kuti apereke nsembeyo paguwa lansembe la Yehova.