3 Kuchokera pa katundu wake, mfumuyo inapereka nsembe zopsereza+ zamʼmawa ndi zamadzulo,+ nsembe zopsereza za Masabata,+ za masiku amene mwezi watsopano waoneka+ ndi za pa nthawi yachikondwerero,+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Yehova.