6 Aisiraeli ndi Ayuda amene ankakhala mʼmizinda ya ku Yuda anabweretsanso chakhumi cha ngʼombe, nkhosa ndiponso cha zinthu zopatulika+ zimene anaziyeretsa kuti zikhale za Yehova Mulungu wawo. Anabweretsa zinthu zimenezi zambiri nʼkuziunjika milumilu.