15 Iye ankayangʼanira Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya ndi Sekaniya, mʼmizinda ya ansembe+ amene anali pa maudindo chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Iwowa ankagawa zinthu kumagulu a abale awo ndipo ankawagawira mofanana,+ kaya akhale wamkulu kapena wamngʼono.