32 Pambuyo pa zimenezi ndiponso pambuyo pa zinthu zokhulupirika+ zimene Hezekiya anachitazi, Senakeribu mfumu ya Asuri anabwera kuti adzaukire Yuda. Iye anamanga misasa pafupi ndi mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri nʼcholinga choti alowe nʼkulanda mizindayo.+