5 Kuwonjezera pamenepo, iye anachita zinthu mwakhama ndipo anamanga mpanda umene unagumuka. Anamanganso nsanja mʼmalo osiyanasiyana pamwamba pa mpandawo ndipo kunja kwake anamangako mpanda wina. Anakonzanso Chimulu cha Dothi+ cha mu Mzinda wa Davide ndipo anapanga zishango ndi zida zina zambiri.