21 Ndiyeno Yehova anatumiza mngelo yemwe anapha msilikali aliyense wamphamvu,+ mtsogoleri ndiponso mkulu wa asilikali aliyense mumsasa wa mfumu ya Asuri, moti mfumuyo inabwerera kwawo mwamanyazi. Kenako inalowa mʼkachisi wa mulungu wake ndipo ena mwa ana ake anaipha ndi lupanga mʼkachisimo.+