33 Kenako Hezekiya, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda pachitunda chopita kumanda a ana a Davide.+ Ndipo Ayuda onse ndi anthu a ku Yerusalemu anamulemekeza kwambiri pa maliro ake. Ndiyeno mwana wake Manase anakhala mfumu mʼmalo mwake.