3 Mʼchaka cha 8 cha ulamuliro wake, akadali mnyamata, Yosiya anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide kholo lake.+ Mʼchaka cha 12 anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu+ pochotsa malo okwezeka,+ mizati yopatulika, zifaniziro zogoba+ ndiponso zifaniziro zachitsulo.