8 Akalonga ake anaperekanso nsembe yaufulu kwa anthuwo, kwa ansembe ndi kwa Alevi. Hilikiya,+ Zekariya ndi Yehiela monga atsogoleri a nyumba ya Mulungu woona, anapereka kwa ansembe nkhosa ndi mbuzi zokwana 2,600 ndiponso ngʼombe 300 kuti zikhale nsembe za Pasika.