23 “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse apadziko lapansi.+ Iye wandituma kuti ndimumangire nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda.+ Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Yehova Mulungu wake akhale naye ndipo apite.’”+