3 Koma Zerubabele, Yesuwa ndi atsogoleri ena onse a nyumba za makolo za Isiraeli anawayankha kuti: “Sizingatheke kuti timange nyumba ya Mulungu wathu limodzi ndi inu.+ Timanga tokha nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, mogwirizana ndi zimene Mfumu Koresi ya Perisiya yatilamula.”+