13 Ndiyeno inu mfumu dziwani kuti, mzinda umenewu ukamangidwanso, mpanda wake nʼkumalizidwa, anthu amenewa asiya kupereka msonkho umene munthu aliyense amapereka, msonkho wakatundu+ ndi msonkho wamsewu ndipo zimenezi zidzachititsa kuti chuma cha mafumu chiwonongeke.