3 “Mʼchaka choyamba cha Mfumu Koresi, mfumuyo inaika lamulo lokhudza nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu lakuti:+ ‘Ayuda amangenso nyumbayo kuti azikapereka nsembe kumeneko ndipo amange maziko olimba. Nyumbayo ikhale mikono 60 kupita mʼmwamba ndiponso mikono 60 mulifupi mwake.+