25 Iweyo Ezara, pogwiritsa ntchito nzeru zimene Mulungu wako wakupatsa, uike akuluakulu a zamalamulo ndi oweruza kuti nthawi zonse aziweruza anthu onse akutsidya la Mtsinje komanso onse odziwa malamulo a Mulungu wako. Aliyense amene sadziwa malamulowo, uzimuphunzitsa.+