28 Iye wandisonyeza chikondi chokhulupirika pamaso pa mfumu,+ pamaso pa alangizi ake+ ndiponso pamaso pa akalonga onse amphamvu a mfumu. Ineyo ndinalimba mtima chifukwa dzanja la Yehova Mulungu wanga linkandithandiza, ndipo ndinasonkhanitsa atsogoleri a Aisiraeli kuti tipitire limodzi.