18 Popeza dzanja labwino la Mulungu wathu linkatithandiza, iwo anatibweretsera munthu wanzeru wochokera pakati pa ana a Mali+ mdzukulu wa Levi mwana wa Isiraeli. Dzina lake linali Serebiya+ ndipo anabwera limodzi ndi ana ake komanso abale ake. Onse pamodzi analipo 18.