13 Usikuwo ndinatulukira pa Geti ya Kuchigwa+ nʼkukadutsa kutsogolo kwa Kasupe wa Chinjoka Chachikulu mpaka ndinakafika ku Geti ya Milu ya Phulusa.+ Pa nthawiyi, ndinkaona mmene mpanda wa Yerusalemu unawonongekera ndiponso mmene moto unawonongera mageti ake.+