4 Meremoti+ mwana wa Uliya, mwana wa Hakozi, anakonza mpandawo kuchokera pamene ana a Haseneya analekezera. Mesulamu+ mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele, anapitiriza kuchokera pamene Meremoti analekezera. Ndipo Zadoki mwana wa Baana, anapitiriza kuchokera pamene Mesulamu analekezera.