8 Munamuona kuti anali ndi mtima wokhulupirika,+ choncho munachita naye pangano kuti mudzamʼpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ayebusi ndi Agirigasi. Munalonjeza kuti mudzapereka dziko limeneli kwa mbadwa+ zake ndipo munakwaniritsadi zimene munalonjeza chifukwa ndinu wolungama.