10 Ndiyeno munakhaulitsa Farao, atumiki ake onse ndiponso anthu onse amʼdziko lake powaonetsa zizindikiro ndi zodabwitsa.+ Munachita zimenezi chifukwa munadziwa kuti iwo anachita zinthu modzikuza+ kwa makolo athu. Pamenepa munadzipangira dzina lomwe lilipobe mpaka lero.+