27 Chifukwa cha zimenezi, munawapereka mʼmanja mwa adani awo+ amene ankawazunza.+ Koma akakumana ndi mavuto ankakulirirani ndipo inu munkamva muli kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chachikulu, munkawapatsa anthu oti awapulumutse mʼmanja mwa adani awo.+