28 Koma akangokhala pamtendere ankachitanso zoipa pamaso panu+ ndipo munkawapereka mʼmanja mwa adani awo amene ankawapondereza.+ Zikatero, ankabwereranso kwa inu nʼkupempha thandizo+ ndipo inu munkamva muli kumwambako nʼkuwapulumutsa mobwerezabwereza chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+