39 Chifukwa Aisiraeli ndi Alevi ayenera kubweretsa zopereka+ zambewu, vinyo watsopano ndi mafuta+ kuzipinda zosungira katundu. Kumeneku nʼkumene kuli ziwiya zakumalo opatulika, ansembe amene amatumikira, alonda apageti ndiponso oimba. Sitidzanyalanyaza nyumba ya Mulungu wathu.+