25 Choncho ndinawadzudzula ndiponso kuwatemberera. Ena mwa amunawa ndinawamenya+ komanso kuwazula tsitsi ndipo ndinawalumbiritsa pamaso pa Mulungu kuti: “Musapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna, ndipo musalole kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna kapenanso inuyo.+