19 Ngati mungavomereze mfumu, mupereke lamulo ndipo lamuloli lilembedwe mʼmalamulo a Perisiya ndi Mediya omwe sasintha.+ Mulamule kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso panu, inu Mfumu Ahasiwero, ndipo mupereke udindo wake kwa mkazi wina, wabwino kuposa iyeyo.