5 Panali munthu wina, Myuda, amene ankakhala kunyumba ya mfumu ya ku Susani+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Dzina lake anali Moredikayi.+ Moredikayi anali mwana wa Yairi, Yairi anali mwana wa Simeyi ndipo Simeyi anali mwana wa Kisi wa fuko la Benjamini.+