7 Moredikayi ndi amene ankalera Hadasa, amene ndi Esitere, mwana wa achimwene awo a bambo ake,+ chifukwa analibe bambo kapena mayi. Mtsikanayu anali wooneka bwino ndiponso wokongola kwambiri. Bambo ndi mayi a mtsikanayu atamwalira, Moredikayi anamʼtenga nʼkumakhala naye ngati mwana wake.