-
Esitere 2:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Mtsikanayo ankapita kwa mfumu madzulo nʼkubwerako mʼmawa ndipo ankapita kunyumba yachiwiri ya akazi, imene Sasigazi ankayangʼanira. Sasigazi anali munthu wofulidwa wa mfumu+ yemwe ankayangʼanira akazi aangʼono* a mfumu. Mtsikanayo sankapitanso kwa mfumu pokhapokha ngati mfumuyo yasangalala naye ndipo yamuitanitsa pomutchula dzina.+
-