-
Esitere 2:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Esitere anali mwana wa Abihaili, mchimwene wawo wa bambo ake a Moredikayi. Moredikayi anamutenga nʼkumakhala naye ngati mwana wake.+ Ndiyeno nthawi yoti Esitere akaonekere kwa mfumu itakwana, sanapemphe kalikonse kupatulapo zimene Hegai anamuuza. Hegai anali munthu wofulidwa wa mfumu amenenso ankayangʼanira akazi. (Pa nthawi yonseyi aliyense womuona Esitere ankamukonda.)
-