16 “Pitani mukasonkhanitse Ayuda onse amene ali ku Susani ndipo musale kudya+ mʼmalo mwa ine. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu,+ masana ndiponso usiku. Inenso ndi atsikana onditumikira tisala kudya. Ngakhale kuti ndi zosemphana ndi lamulo, ndidzapita kwa mfumu ndipo ngati nʼkufa, ndife.”