13 Hamani atafotokozera mkazi wake Zeresi+ ndiponso anzake onse zonse zimene zinamuchitikira, amuna anzeru amene ankamutumikira komanso mkazi wakeyo anati: “Ngati wayamba kufooka pamaso pa Moredikayi, yemwe ndi Myuda, ndiye kuti supambana koma akugonjetsa ndithu.”