9 Ndiyeno Haribona,+ mmodzi mwa nduna zapanyumba ya mfumu, anati: “Hamani anapanganso mtengo woti apachikepo Moredikayi,+ amene anapereka lipoti lomwe linapulumutsa mfumu.+ Mtengowo ndi wautali mikono 50 ndipo uli kunyumba kwa Hamani.” Zitatero mfumu inati: “Kamʼpachikeni pamtengo womwewo.”