10 Moredikayi analemba makalatawo mʼdzina la Mfumu Ahasiwero nʼkuwadinda ndi mphete yodindira ya mfumu.+ Atatero anatumiza makalatawo kudzera mwa anthu operekera makalata okwera pamahatchi. Iwo anapita pamahatchi aliwiro amene ankawagwiritsa ntchito potumikira mfumu.