14 Anthu operekera makalatawo anapita mofulumira atakwera pamahatchi amene ankawagwiritsa ntchito potumikira mfumu ndipo anachita zimenezi chifukwa cha lamulo la mfumu. Lamuloli linaperekedwanso kunyumba ya mfumu ya ku Susani+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.