10 Sindinadzimane chilichonse chimene mtima wanga unkalakalaka.+ Mtima wanga sindinaumane zosangalatsa za mtundu uliwonse. Ndinkasangalala chifukwa cha ntchito yonse imene ndinagwira mwakhama. Imeneyi inali mphoto yanga pa ntchito yonse imene ndinagwira mwakhama.+