4 Ine ndinaganiziranso zinthu zonse zimene anthu amachita akamapondereza anzawo padziko lapansi pano. Ndinaona anthu oponderezedwa akugwetsa misozi, koma panalibe aliyense woti awatonthoze.+ Anthu oponderezawo anali ndi mphamvu, moti panalibe aliyense woti atonthoze anthu oponderezedwawo.