14 Pali chinthu china chachabechabe chimene chimachitika padziko lapansi: Pali anthu olungama amene amachitiridwa zinthu ngati kuti achita zoipa,+ ndipo pali anthu oipa amene amachitiridwa zinthu ngati kuti achita zachilungamo.+ Ndikunena kuti zimenezinso nʼzachabechabe.