8 Tiye tichokere limodzi ku Lebanoni, iwe mkwatibwi wanga,
Tiye tichokere limodzi ku Lebanoni.+
Utsetsereke kuchokera pamwamba pa phiri la Amana,
Kuchokera pamwamba pa phiri la Seniri, kapena kuti pamwamba pa phiri la Herimoni.+
Utsetsereke kuchokera mʼmapanga a mikango, ndiponso kuchokera kumapiri a akambuku.