9 Koma mmodzi yekha ndi amene ali njiwa yanga,+ wopanda chilema.
Iye ndi mwana wapadera kwambiri kwa mayi ake.
Ndi mwana amene amakondedwa ndi mayi amene anamubereka.
Ana aakazi akamuona, amamunena kuti ndi wosangalala.
Mafumukazi ndi adzakazi amamutamanda.