5 malo onse a paphiri la Ziyoni ndi malo onse a mu Yerusalemu ochitirapo misonkhano, Yehova adzawapangira mtambo ndi utsi kuti ziziwathandiza masana. Adzawapangiranso moto wowala walawilawi kuti uziwathandiza usiku,+ ndipo pamwamba pa malo onse aulemererowo padzakhala chotchinga.