2 Anthu a mitundu ina adzawatenga nʼkubwerera nawo kwawo ndipo nyumba ya Isiraeli idzatenga anthuwo kuti akhale antchito awo aamuna ndi aakazi+ mʼdziko la Yehova. Iwo adzagwira anthu amene anawagwira nʼkupita nawo kudziko lina ndipo azidzalamulira anthu amene ankawagwiritsa ntchito mokakamiza.