-
Yesaya 18:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Dzikolo limatumiza nthumwi zake kudzera panyanja,
Zimadutsa pamadzi mʼngalawa zopangidwa ndi gumbwa.* Dzikolo limanena kuti:
“Pitani, inu amithenga achangu,
Ku mtundu wa anthu ataliatali komanso akhungu losalala,
Kwa anthu amene kulikonse amaopedwa,+
Kwa mtundu wa anthu amphamvu, amene akugonjetsa mitundu ina,
Umene nthaka yake yakokoloka ndi mitsinje.”
-