2 Pa nthawi imeneyo Yehova analankhula kudzera mwa Yesaya+ mwana wa Amozi kuti: “Pita ukavule chiguduli chimene chili mʼchiuno mwako komanso nsapato zimene zili kuphazi kwako.” Iye anachitadi zimenezo, nʼkumayenda ali maliseche ndiponso wopanda nsapato.