4 Mofanana ndi zimenezi, mfumu ya Asuri idzagwira gulu la anthu ku Iguputo+ ndi ku Itiyopiya nʼkupita nawo ku ukapolo kudziko lina. Idzagwira anyamata ndi amuna achikulire, ali opanda zovala ndi opanda nsapato, ndiponso matako awo ali pamtunda moti Iguputo adzachititsidwa manyazi.