9 Pa tsiku limenelo anthu akewo adzanena kuti:
“Taonani! Uyu ndi Mulungu wathu.+
Chiyembekezo chathu chinali mwa iye+
Ndipo iye watipulumutsa.+
Uyu ndi Yehova.
Chiyembekezo chathu chinali mwa iye.
Tiyeni tisangalale ndi kukondwera chifukwa watipulumutsa.”+